-
Yesaya 30:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Uwu ndi uthenga wokhudza zilombo zokhala kumʼmwera:
Podutsa mʼdziko la mavuto ndi la zowawa,
La mkango, mkango umene ukubangula,
La mphiri ndi la njoka zouluka zaululu wamoto,*
Iwo anyamula chuma chawo pamsana pa abulu
Ndiponso katundu wawo pamalinunda a ngamila.
Koma anthuwo sadzapindula ndi zinthu zimenezi.
-