2 Kenako mfumu ya Asuri inatumiza Rabisake+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Inamutumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali. Iwo anakaima pafupi ndi ngalande yochokera kudziwe lakumtunda,+ limene lili pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+