9 Mitundu yonse isonkhane pamalo amodzi,
Ndipo mitundu ya anthu isonkhanitsidwe pamodzi.+
Ndi ndani pakati pa milungu yawo amene ananena kuti zinthu zimenezi zidzachitika?
Kapena kodi angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+
Abweretse mboni zawo kuti tidziwe ngati akunena zoona,
Kapena mbonizo zimvetsere nʼkunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+