13 Mmisiri wosema mtengo watambasula chingwe choyezera. Walemba mtengowo ndi choko chofiira.
Wausema ndi sompho ndipo waulemberera ndi chipangizo cholembera mizere yozungulira.
Waupanga kuti uzioneka ngati munthu,+
Waukongoletsa ngati munthu,
Kuti uzikhala mʼnyumba.+