21 Ndipo mumtima mwako udzanena kuti,
‘Kodi bambo amene wandiberekera anawa ndi ndani,
Popeza ine ndine mayi woferedwa ana ndiponso amene anasiya kubereka,
Mayi amene anatengedwa kupita kudziko lina kuti akakhale mkaidi?
Inetu ndinangosiyidwa ndekhandekha,+
Ndiye ana amenewa achokera kuti?’”+