23 Mafumu adzakhala okusamalira,+
Ndipo ana awo aakazi adzakhala okuyamwitsira ana ako.
Iwo adzakugwadira mpaka nkhope zawo pansi+
Ndipo adzanyambita fumbi lakumapazi ako.+
Choncho iwe udzadziwa kuti ine ndine Yehova.
Anthu amene amandikhulupirira sadzachita manyazi.”+