13 Ngati chifukwa cha Sabata mukupewa kuchita zofuna zanu pa tsiku langa lopatulika,+
Ndipo mukanena kuti Sabata ndi tsiku losangalatsa kwambiri, tsiku lopatulika la Yehova, tsiku loyenera kulemekezedwa,+
Ndipo mukalilemekeza mʼmalo mochita zofuna zanu ndiponso mʼmalo molankhula zopanda pake,