21 Yehova wanena kuti: “Koma pangano langa ndi iwowo ndi ili,+ mzimu wanga umene uli pa iwe ndi mawu anga amene ndaika mʼkamwa mwako, sizidzachotsedwa mʼkamwa mwako, mʼkamwa mwa ana ako kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zako, kuyambira panopa mpaka kalekale,” akutero Yehova.