30 Popeza tsopano wawonongedwa, ndiye utani?
Unkakonda kuvala zovala zamtengo wapatali,
Kudzikongoletsa ndi zokongoletsera zagolide
Ndiponso kukongoletsa mʼmaso mwako ndi penti wakuda.
Koma unkangotaya nthawi yako pachabe podzikongoletsa.+
Amene ankakufuna akukana
Ndipo tsopano akufuna kukupha.+