20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani! Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zidzatsanulidwa pamalo awa,+ pamunthu, pachiweto, pamitengo yakuthengo ndi pachipatso chilichonse chochokera mʼnthaka. Mkwiyowo udzayaka ndipo sudzazimitsidwa.’+