8 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu. Mʼmalomwake aliyense wa iwo anapitiriza kuumitsa mtima wake ndi kuchita zofuna za mtima wake woipawo.+ Choncho ndinawalanga mogwirizana ndi mawu onse a mʼpangano langa limene ndinawalamula kuti azilitsatira koma iwo anakana kulitsatira.’”