9 Mkazi amene wabereka ana 7 wafooka,
Ndipo akupuma movutikira.
Kwa iye dzuwa lalowa masanasana,
Iye wachita manyazi ndipo wathedwa nzeru.’
Ndipo anthu awo otsala omwe ndi ochepa
Ndidzawapereka kwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,’ akutero Yehova.”+