19 Choncho Yehova wanena kuti:
“Ukabwerera, ine ndidzakukonda,
Ndipo udzapitiriza kunditumikira.
Ukasiyanitsa zinthu zamtengo wapatali ndi zinthu zopanda phindu,
Udzakhala ngati pakamwa panga.
Anthuwo adzayenera kubwera kwa iwe,
Koma iwe sudzapita kwa iwo.”