26 Anthu adzabwera kuchokera mʼmizinda ya Yuda, mʼmadera ozungulira Yerusalemu, mʼdziko la Benjamini,+ kuchigwa,+ mʼdera lamapiri komanso kuchokera ku Negebu. Iwo adzabweretsa kunyumba ya Yehova nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zina,+ nsembe zambewu,+ lubani ndi nsembe zoyamikira.+