18 kuyamba ndi Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda+ komanso mafumu ake ndi akalonga ake. Ndinawamwetsa kuti mizinda yawo ikhale bwinja, chinthu chochititsa mantha chimene anthu azidzachiimbira mluzu ndiponso kuti ikhale yotembereredwa+ ngati mmene zilili lero.