2 “Yehova wanena kuti, ‘Ukaimirire mʼbwalo la nyumba ya Yehova ndipo ukanene zimene zidzachitikire anthu onse amʼmizinda ya Yuda amene akubwera kudzalambira panyumba ya Yehova. Ukawauze zonse zimene ndakulamula ndipo usachotsepo mawu ngakhale amodzi.