16 Ndiyeno ndinauza ansembe ndi anthu onsewo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Musamvere mawu a aneneri anu amene akulosera kwa inu kuti: “Taonani! Ziwiya zamʼnyumba ya Yehova zibwezedwa posachedwapa kuchokera ku Babulo!”+ chifukwa iwo akulosera zabodza kwa inu.+