11 Kenako Hananiya anauza anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndathyolera goli ili, zaka ziwiri zisanathe,+ ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babulo limene waveka mitundu yonse ya anthu.’” Zitatero, mneneri Yeremiya anachokapo.