3 “Taona! masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,” akutero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kuti likhalenso lawo.”’”+