21 ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga+ kuti asakhale ndi mwana woti adzalamulire monga mfumu pampando wake wachifumu wa Davide.+ Ndingachitenso chimodzimodzi ndi pangano langa ndi atumiki anga Alevi omwe ndi ansembe.+