10 Kenako Baruki anawerenga mokweza mpukutu womwe unali ndi mawu a Yeremiya mʼnyumba ya Yehova. Anachita zimenezi mʼchipinda cha Gemariya+ mwana wa Safani+ wokopera Malemba, mʼbwalo limene linali mʼmwamba, pakhomo la geti latsopano la nyumba ya Yehova,+ anthu onse akumva.