12 anapita kunyumba ya mfumu, kuchipinda cha mlembi. Akalonga onse anali atakhala pansi kumeneko ndipo kunali Elisama+ mlembi, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani+ mwana wa Akibori,+ Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya ndi akalonga ena onse.