11 Choncho Ebedi-meleki anatenga amunawo ndipo analowa mʼnyumba ya mfumu, mʼchipinda chimene chinali pansi pa malo osungira chuma.+ Kumeneko anatengako nsanza ndi nsalu zakutha nʼkuzilowetsa mʼchitsime momwe munali Yeremiya pogwiritsa ntchito zingwe.