22 Taonani! Akazi onse amene anatsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda akupita nawo kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ ndipo akaziwo akunena kuti,
‘Amuna amene munkawadalira akuputsitsani ndipo akugonjetsani.+
Achititsa kuti mapazi anu amire mʼmatope
Tsopano akubwerera ndipo akusiyani.’