10 Koma ine ndizikhala ku Mizipa kuno kuti ndizikuimirirani kwa Akasidi amene azibwera kwa ife. Koma inuyo musonkhanitse vinyo, zipatso zamʼchilimwe ndi mafuta nʼkuziika mʼziwiya zanu zosungira zinthu ndipo muzikhala mʼmizinda imene mwaitenga kuti ikhale yanu.”+