41 Mʼmwezi wa 7, Isimaeli+ mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa+ pamodzi ndi amuna ena 10. Isimaeli anali wa mʼbanja lachifumu ndipo analinso mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. Pamene ankadyera limodzi chakudya ku Mizipa,