-
Yeremiya 44:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Mʼmalomwake tichitadi zonse zimene tanena. Tipereka nsembe komanso tithira nsembe zachakumwa kwa Mfumukazi Yakumwamba.*+ Tichita zimenezi mofanana ndi mmene ife, makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu anachitira mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu pamene tinkadya mkate nʼkukhuta ndipo zinthu zinkatiyendera bwino, moti sitinaone tsoka lililonse.
-