8 Yerusalemu wachita tchimo lalikulu.+
Nʼchifukwa chake wakhala chinthu chonyansa.
Anthu onse amene ankamulemekeza ayamba kumuona ngati chinthu chochititsa manyazi, chifukwa aona maliseche ake.+
Iyenso akulira+ ndipo watembenukira kumbali chifukwa cha manyazi.