13 Iye watumiza moto mʼmafupa mwanga+ kuchokera kumwamba ndipo wafooketsa fupa lililonse.
Watchera ukonde kuti ukole mapazi anga. Wandikakamiza kuti ndibwerere mʼmbuyo.
Wandichititsa kuti ndikhale mkazi amene wasiyidwa yekhayekha.
Ndikudwala tsiku lonse.