8 Yehova watsimikiza kuti awononge mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni.+
Watambasula chingwe choyezera.+
Sanabweze dzanja lake kuti lisabweretse chiwonongeko.
Wachititsa kuti malo okwera omenyerapo nkhondo ndi mpanda zilire.
Zonse pamodzi zachititsidwa kuti zisakhalenso ndi mphamvu.