6 Koma iwe mwana wa munthu, usawaope+ ndipo usachite mantha ndi zimene akunena ngakhale kuti wazunguliridwa ndi anthu amene ali ngati minga+ komanso ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena+ ndipo usaope nkhope zawo,+ chifukwa iwo ndi anthu opanduka.