18 Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ koma iwe osalankhula naye nʼkumuchenjeza kuti asiye zoipa zimene akuchita kuti akhalebe ndi moyo,+ munthuyo adzafa chifukwa cha zolakwa zake popeza ndi woipa,+ koma iwe ndidzakuimba mlandu chifukwa cha magazi ake.+