2 Gawo limodzi la magawo atatu a tsitsilo uliwotche pamoto mumzindawo, masiku ozungulira mzindawo akatha.+ Kenako utenge gawo lina la magawo atatuwo nʼkumalimenya ndi lupanga ukuzungulira mzindawo.+ Gawo lomaliza la magawo atatuwo uliuluze ndi mphepo ndipo ine ndilitsatira nditasolola lupanga.+