-
Ezekieli 7:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Siliva wawo adzamutaya mʼmisewu ndipo golide wawo adzanyansidwa naye. Siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku limene Yehova adzasonyeze mkwiyo wake waukulu.+ Golide ndi siliva wawo sadzathetsa njala yawo kapena kuwakhutitsa, chifukwa chumacho chakhala ngati chinthu chopunthwitsa chimene chawachititsa kuti achimwe.
-