27 Mfumu idzayamba kulira+ ndipo mtsogoleri adzagwidwa ndi mantha. Manja a anthu amʼdzikolo adzanjenjemera chifukwa cha mantha. Ndidzawachitira zinthu zogwirizana ndi njira zawo ndipo ndidzawaweruza mogwirizana ndi mmene ankaweruzira ena. Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+