6 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zinthu zoipa komanso zonyansa kwambiri zimene anthu a nyumba ya Isiraeli akuchita kuno,+ zimene zikupangitsa kuti nditalikirane ndi malo anga opatulika?+ Koma uonanso zinthu zina zoipa zomwe ndi zonyansa kwambiri kuposa zimenezi.”