17 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi? Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti anthu a nyumba ya Yuda azichita zinthu zonyansazi? Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti adzaze dzikoli ndi chiwawa+ nʼkupitiriza kundikwiyitsa? Anthuwatu akulozetsa nthambi pamphuno panga.