3 Kenako ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli+ unachoka pamwamba pa akerubi pamene unali ndipo unapita pakhomo la malo opatulika.+ Ndiyeno Mulungu anayamba kulankhula mofuula kwa munthu amene anavala zovala zansalu uja, yemwe mʼchiuno mwake munali kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera.