9 Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda nʼzazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi kukhetsa magazi+ ndipo mumzindamo mwadzaza zinthu zopanda chilungamo.+ Iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo mʼdziko muno ndipo Yehova sakuona.’+