19 Tsopano akerubi aja anakweza mʼmwamba mapiko awo nʼkunyamuka kuchoka pansi ine ndikuona. Pamene amanyamuka, mawilo aja anali pambali pawo. Kenako iwo anakaima pakhomo lakumʼmawa la geti la nyumba ya Yehova ndipo ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pawo.+