19 Inu mukundinyozetsa pamaso pa anthu anga chifukwa cha balere wongodzaza mʼmanja ndi nyenyeswa za mkate.+ Inu mukupha anthu amene sakuyenera kufa, ndipo mukusiya anthu amene sakuyenera kukhala ndi moyo. Mukuchita zimenezi ponamiza anthu anga amene akumvetsera mabodza anuwo.”’+