8 ‘Ndikudutsa pafupi ndinakuona ndipo ndinazindikira kuti wafika pamsinkhu woti utha kuyamba kukondana ndi munthu. Choncho ndinakuphimba ndi chovala changa+ ndipo ndinabisa maliseche ako. Ndinalumbira nʼkuchita nawe pangano ndipo unakhala wanga,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.