13 Unapitiriza kudzikongoletsa ndi zinthu zagolide ndi zasiliva. Zovala zako zinali za nsalu zabwino kwambiri, nsalu zamtengo wapatali komanso chovala cha nsalu yopeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta ndipo unakhala wokongola kwambiri+ moti unali woyenera kukhala mfumukazi.