27 Tsopano ine nditambasula dzanja langa nʼkukulanga ndipo ndichepetsa chakudya chimene ndimakupatsa.+ Ndikupereka kwa akazi amene amadana nawe+ kuti achite nawe zimene akufuna. Ndikupereka kwa ana aakazi a Afilisiti, amene ankanyansidwa ndi khalidwe lako lonyansa.+