36 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa wasonyeza chilakolako mopitirira muyezo ndipo maliseche ako aonekera pamene umachita zauhule ndi zibwenzi zako ndiponso mafano ako onse onyansa,+ amene unafika powapatsa nsembe za magazi a ana ako,+