3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ku Lebanoni+ kunabwera chiwombankhanga chachikulu+ cha mapiko akuluakulu komanso ataliatali. Chiwombankhangacho chinali ndi nthenga zambiri zamitundu yosiyanasiyana. Chitafika kumeneko, chinathyola nsonga ya mtengo wa mkungudza.+