8 Koma iwo anandipandukira ndipo sanafune kundimvera. Iwo sanataye zinthu zonyansa zimene ankazitumikira ndipo sanasiye kulambira mafano onyansa a ku Iguputo.+ Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuti ndiwatsanulire mkwiyo wanga komanso kuwaonetsa ukali wanga wonse mʼdziko la Iguputo.