12 Lira ndi kufuula+ iwe mwana wa munthu, chifukwa lupangalo labwera kuti lidzaphe anthu anga. Labwera kudzapha atsogoleri onse a Isiraeli.+ Atsogoleriwa adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Choncho menya pantchafu pako chifukwa cha chisoni.