26 Ansembe ako aphwanya chilamulo changa+ ndipo akupitiriza kuipitsa malo anga oyera.+ Sakusiyanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba+ ndipo akulephera kuuza anthu kuti zinthu zodetsedwa ndi ziti komanso zinthu zoyera ndi ziti.+ Iwo akukana kusunga sabata langa ndipo adetsa dzina langa pakati pawo.