25 Ndidzasonyeza mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga mwaukali. Adzakudula mphuno ndi makutu ndipo ena a inu amene adzatsale adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzatenga ana ako aamuna ndi aakazi ndipo anthu ena amene adzatsale adzawotchedwa ndi moto.+